Psalms 77

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a Yedutuni. Salimo la Asafu.

1Ndinafuwulira Mulungu kupempha thandizo;
ndinafuwula mokweza kwa Mulungu kuti anditcherere khutu.
2Pamene ndinali pa masautso ndinafunafuna Ambuye;
usiku ndinatambasula manja mosalekeza
ndipo moyo wanga unakana kutonthozedwa.

3Ndinakumbukira Inu Mulungu, ndipo ndinabuwula;
ndinasinkhasinkha ndipo mzimu wanga unalefuka.
Sela
4Munagwira zikope zanga kuti ndisagone
ndipo ndinavutika kwambiri kuti ndiyankhule.
5Ndinaganizira za masiku akale,
zaka zamakedzana;
6Ndinakumbukira nyimbo zanga usiku.
Mtima wanga unasinkhasinkha ndipo mzimu wanga unafunsa kuti,

7“Kodi Ambuye adzatikana mpaka muyaya?
Kodi Iwo sadzaonetsanso kukoma mtima kwawo?
8Kodi Chikondi chake chosatha chija chatheratu?
Kodi malonjezo ake alephera nthawi yonse?
9Kodi Mulungu wayiwala kukhala wokoma mtima?
Kodi mu mkwiyo wake waleka chifundo chake?”

10Ndipo ndinaganiza, “Pa izi ine ndidzapemphanso:
zaka za dzanja lamanja la Wammwambamwamba.
11Ine ndidzakumbukira ntchito za Yehova;
Ine ndidzakumbukira zodabwitsa zanu za kalekale.
12Ndidzakumbukira ntchito zanu
ndi kulingalira zodabwitsa zanu.”

13Njira zanu Mulungu ndi zoyera.
Kodi ndi mulungu uti ali wamkulu kuposa Mulungu wathu?
14Inu ndinu Mulungu wochita zodabwitsa;
Mumaonetsera mphamvu yanu pakati pa mitundu ya anthu.
15Ndi dzanja lanu lamphamvu munawombola anthu anu,
zidzukulu za Yakobo ndi Yosefe.
Sela

16Madzi anakuonani Mulungu,
madzi anakuonani ndipo anachita mantha;
nyanja yozama inakomoka.
17Mitambo inakhuthula madzi ake pansi,
mu mlengalenga munamveka mabingu;
mivi yanu inawuluka uku ndi uku.
18Bingu lanu linamveka mʼmphepo ya kamvuluvulu,
mphenzi yanu inawalitsa dziko lonse;
dziko lapansi linanjenjemera ndi kugwedezeka.
19Njira yanu inadutsa pa nyanja,
njira yanu inadutsa pa madzi amphamvu,
ngakhale zidindo za mapazi anu sizinaoneke.

20Inu munatsogolera anthu anu ngati gulu la nkhosa
mwa dzanja la Mose ndi Aaroni.
Copyright information for NyaCCL